1 Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanzaKhristu.
Za akazi mu Mpingo wa Ambuye
2 Ndipo ndikutamandani kuti m’zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.
3 Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.
4 Mwamuna yense woveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake.
5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.
6 Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.
7 Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.
8 Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;
9 pakutinso mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi;
10 koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa chaangelo.
11 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.
12 Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu.
13 Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?
14 Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chinyozetsa iye?
15 Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.
16 Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapenaMpingowa Mulungu.
Zosayenera pa madyerero a chikondi. Machitidwe a Mgonero wa Ambuye
17 Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa.
18 Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndivomereza penapo.
19 Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.
20 Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;
21 pakuti pakudyaku yense ayamba watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.
22 Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m’menemo? Sindikutamani.
23 Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;
24 ndipo m’mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.
25 Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa.
26 Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.
27 Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.
28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho.
29 Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.
30 Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.
31 Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa.
32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.
33 Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.
34 Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/11-3a196396f2b1e62185a8dd66e86996d8.mp3?version_id=1068—