Tisayese dala Mulungu monga Israele
1 Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
2 nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m’nyanja,
3 nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;
4 namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiyeKhristu.
5 Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwere nao; pakuti anamwazika m’chipululu.
6 Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.
7 Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.
8 Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.
9 Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.
10 Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.
11 Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.
12 Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.
13 Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Za kupembedza mafano, za kuyanjana ndi ziwanda
14 Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.
15 Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena.
16 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?
17 Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.
18 Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?
19 Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi?
20 Koma nditi kuti zimeneamitunduapereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.
21 Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.
22 Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?
Mkhristu ndiye mfulu koma wosamalira ena
23 Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.
24 Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.
25 Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbumtima;
26 pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.
27 Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbumtima.
28 Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbumtima.
29 Ndinena chikumbumtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbumtima cha wina?
30 Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo?
31 Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
32 Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapenaMpingowa Mulungu;
33 monga inenso ndikondweretsa onse m’zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/10-7ee5c8f016dffdb4a67765fd2cac3f0f.mp3?version_id=1068—